1 Samueli 25:34 - Buku Lopatulika34 Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundichingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutacha kanthu konse, ngakhale mwana wamwamuna mmodzi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201434 Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundichingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutacha kanthu konse, ngakhale mwana wamwamuna mmodzi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa34 Chauta, Mulungu wa Israele, ndiye wandiletsa kuti ndisakupwetekeni. Zoonadi, pali Chauta, Mulungu wamoyo, mukadapanda kudzakumana nane msanga, ndithu sipakadamtsalira Nabala munthu wamwamuna ndi mmodzi yemwe maŵa m'maŵa.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero34 Kunena zoona, pali Yehova Wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene wandiletsa kuti ndisakupwetekeni, mukanapanda kubwera msanga kudzakumana nane, palibe munthu aliyense wamwamuna wa Nabala akanasiyidwa wamoyo pakucha mmawa.” Onani mutuwo |
Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake.