1 Samueli 25:18 - Buku Lopatulika18 Pomwepo Abigaile anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zowotchaotcha, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi nchinchi za mphesa zouma zana limodzi, ndi nchinchi za nkhuyu mazana awiri, naziika pa abulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Pomwepo Abigaile anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zoochaocha, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi nchinchi za mphesa zouma zana limodzi, ndi nchinchi za nkhuyu mazana awiri, naziika pa abulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Tsono mwamsanga Abigaile adatenga mitanda yabuledi 200, matumba achikopa aŵiri a vinyo, nkhosa zisanu zootcheratu, makilogramu 17 a tirigu wokazinga, nchinchi za mphesa zoumika 100, ndiponso makeke ankhuyu 200. Zonsezo adazisenzetsa abulu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Ndipo Abigayeli sanataye nthawi. Iye anatenga malofu a buledi 200, matumba a chikopa awiri a vinyo, nkhosa zisanu zowotcheratu, makilogalamu 17 a tirigu wokazinga, makeke a mphesa zowuma 100, ndiponso makeke a nkhuyu 200, ndipo anazisenzetsa abulu. Onani mutuwo |