Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 25:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Davide anati kwa anthu ake, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lake. Namangirira munthu yense lupanga lake; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lake; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Davide anati kwa anthu ake, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lake. Namangirira munthu yense lupanga lake; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lake; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Apo Davide adauza ankhondo ake kuti, “Munthu aliyense amangirire lupanga lake.” Choncho aliyense adamangirira lupanga lake. Davide nayenso adamangirira lake. Anthu amene adapita ndi Davide analipo ngati 400. Koma anthu 200 adatsalira kuti azisunga katundu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Davide anawuza anthu ake kuti, “Aliyense amangirire lupanga lake!” Choncho aliyense anamangirira lupanga lake. Davidenso anamangirira lupanga lake. Anthu pafupifupi 400 ndiwo anapita ndi Davide, pamene anthu 200 anatsala ndi katundu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:13
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anyamata ake onse anapita naye limodzi; ndi Akereti ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kuchokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu.


Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru.


Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mzinda.


Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.


Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino; ndipo wofulumira ndi mapazi ake amachimwa.


Usanene, Ndidzabwezera zoipa; yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.


Usatuluke mwansontho kukalimbana, ungalephere pa kutha kwake, atakuchititsa mnzako manyazi.


Pamenepo amunawo analandirako kamba wao, osafunsira pakamwa pa Yehova.


Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai.


Potero Davide ndi anyamata ake, ndiwo monga ngati mazana asanu ndi limodzi, ananyamuka, natuluka ku Keila, nayendayenda kulikonse adakhoza kuyendako. Ndipo anauza Saulo kuti Davide wapulumuka ku Keila; iye naleka kumtsata.


Chomwecho anyamata a Davide anatembenukira ku njira yao, nabwerera, nadza namuuza monga mwa mau onse awa.


Ndipo Davide ananyamuka, naoloka pamodzi ndi anthu mazana asanu ndi limodzi amene anali naye, nafika kwa Akisi mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa