Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 20:29 - Buku Lopatulika

29 nati, Ndiloleni, ndimuke; chifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mzindamo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndichoke, ndikaone abale anga. Chifukwa cha ichi safika ku gome la mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 nati, Ndiloleni, ndimuke; chifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mudzimo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndichoke, ndikaone abale anga. Chifukwa cha ichi safika ku gome la mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Adati, ‘Undilole ndipite, popeza kuti banja lathu likupereka nsembe mumzindamo, ndipo mbale wanga adandikakamiza kuti ndikakhale nao kumeneko. Tsono ngati wandikomera mtima, undilole ndipite, kuti ndikaone abale anga.’ Nchifukwa chake sadabwere ku chakudya cha mfumu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Anati, ‘Undilole ndipite, chifukwa banja lathu likupereka nsembe mu mzindamo ndipo mʼbale wanga wandiwumiriza kuti ndikakhale nawo. Ngati wandikomera mtima, chonde ndilole ndipite ndikaone abale anga.’ Nʼchifukwa chake sanabwere kudzadya ndi mfumu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 20:29
4 Mawu Ofanana  

Ndipo Samuele anati, Ndikamuka bwanji? Saulo akachimva, adzandipha. Ndipo Yehova anati, Umuke nayo ng'ombe yaikazi, nunene kuti, Ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova.


Ndipo Eliabu mkulu wake anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliyabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? Ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'chipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi.


Ndipo Yonatani anayankha Saulo, Davide anandiumiriza ndimlole amuke ku Betelehemu;


Pamenepo Saulo anapsa mtima ndi Yonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Yeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa