Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 2:8 - Buku Lopatulika

8 Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Amakweza osauka kuŵachotsa pa fumbi, amachotsa anthu osoŵa pa dzala, amaŵakhazika pamodzi ndi akalonga, amaŵapatsa mpando waulemu. Nsanamira za dziko lapansi nzake za Chauta, adakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi, ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala. Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu, amawapatsa mpando waulemu. “Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova, anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 2:8
31 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao anatumiza nakaitana Yosefe; ndipo anamtulutsa iye msanga m'dzenjemo: ndipo iye anameta, nasintha malaya ake, nalowa kwa Farao.


Uziyang'anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mau ako; pa mpando wachifumu pokha ine ndidzakuposa iwe.


Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele.


Popeza ndinakukuza iwe kuchokera kufumbi, ndi kukuika iwe mfumu ya anthu anga Israele, koma iwe unayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi kuchimwitsa anthu anga Israele, kuputa mkwiyo wanga ndi machimo ao;


Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pake, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisraele.


nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.


Ndipo anadzitengera phale, kudzikanda nalo; nakhala pansi m'maphulusa.


Munakhazika dziko lapansi kalelo; ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu.


anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka kunthawi yonse.


Koma aika waumphawi pamsanje posazunzika, nampatsa mabanja ngati gulu la nkhosa.


Pakuti Iye analimanga pazinyanja, nalikhazika pamadzi.


Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo; ndinachirika mizati yake.


Ndinati kwa odzitamandira, musamachita zodzitamandira; ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;


Pakuti Mulungu ndiye woweruza; achepsa wina, nakuza wina.


Pakuti atuluka m'nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m'dziko lake asauka.


Ndipo ndidzamkhomera iye ngati chikhomo cholimba; ndipo iye adzakhala mpando wa ulemerero wa banja la atate wake.


Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni.


Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.


Pamenepo Daniele amene anaposa akuluwa ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang'anira ufumu wonse.


ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,


Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.


Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzachita ufumu kunthawi za nthawi.


Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinapambana, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.


ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.


Nati Samuele, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwe mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa