1 Samueli 17:25 - Buku Lopatulika25 Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeretsa ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu mu Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeza ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu m'Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Ankati, “Muwonenitu munthu uja! Amangobwera, amangodzatinyoza Aisraelefe. Tsono amene amuphe, mfumu idati idzampatsa chuma chambiri, adzampatsanso mwana wake wamkazi kuti amkwatire. Banja la bambo wake silidzalipiranso msonkho.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Ndipo Aisraeli ankanena kuti, “Kodi mwamuona munthu akubwerayo? Iye amangobwera kudzanyoza Israeli. Tsono mfumu inati kuti idzapereka chuma chambiri kwa munthu amene adzamuphe. Idzaperekanso mwana wake wamkazi kuti amukwatire ndiponso banja la abambo ake silidzaperekanso msonkho mu Israeli.” Onani mutuwo |