Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 17:1 - Buku Lopatulika

1 Pamenepo Afilisti anasonkhanitsa makamu ao a nkhondo, naunjikana ku Soko wa ku Yuda, namanga zithando pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamenepo Afilisti anasonkhanitsa makamu ao a nkhondo, naunjikana ku Soko wa ku Yuda, namanga zithando pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo ku Soko, m'dziko la Yuda. Adamanga zithando zao pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Afilisti anasonkhanitsa ankhondo awo ku Soko mʼdziko la Yuda. Iwo anamanga misasa yawo ku Efesi-Damimu, pakati pa Soko ndi Azeka.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 17:1
11 Mawu Ofanana  

Anali pamodzi ndi Davide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti.


ndi Betezuri, ndi Soko, ndi Adulamu,


Afilisti omwe adagwa m'mizinda ya kuchidikha, ndi ya kumwera kwa Yuda, nalanda Betesemesi, ndi Ayaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi midzi yake, ndi Timna ndi midzi yake, ndi Gimizo ndi midzi yake; nakhala iwo komweko.


pamene nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni inamenyana ndi Yerusalemu, ndi mizinda yonse ya Yuda imene inatsala, ndi Lakisi ndi Azeka; pakuti mizinda ya Yuda yamalinga yotsala ndi imeneyi.


Yaramuti, ndi Adulamu, Soko, ndi Azeka;


anasiya mafumu asanu a Afilisti ndi Akanani onse, ndi Asidoni, ndi Ahivi okhala m'phiri la Lebanoni, kuyambira phiri la Baala-Heremoni mpaka polowera ku Hamati.


Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.


Ndipo Saulo analeka kuwapirikitsa Afilistiwo; ndi Afilistiwo anamuka ku malo a iwo okha.


Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Saulo; ndipo Saulo pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye.


Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisraele anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisraele. Ndipo Aisraele pakumva ichi, anachita mantha ndi Afilistiwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa