Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 14:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Saulo ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, natulukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzake ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Saulo ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, natulukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzake ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Pamenepo Saulo pamodzi ndi anthu amene anali naye adasonkhananso napita kukamenya nkhondo, ndipo adaona Afilisti akungophana okhaokha. Motero kunali chisokonezo chachikulu kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Ndipo Sauli ndi asilikali onse amene anali naye anasonkhana kupita kukamenya nkhondo, ndipo anangoona chisokonezo chachikulu kwambiri. Afilisti akuphana okhaokha.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 14:20
8 Mawu Ofanana  

Tsono mfumu ya Israele inatuluka, nikantha apakavalo ndi apamagaleta, nawapha Aaramuwo maphedwe aakulu.


Pakuti ana a Amoni, ndi a Mowabu, anaukira okhala m'phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwaononga psiti; ndipo atatha okhala mu Seiri, anasandulikirana kuonongana.


Ndipo ndidzapikisanitsa Aejipito; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wake, ndi wina ndi mnansi wake; mzinda kumenyana ndi mzinda, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.


Ndipo ndidzamuitanira lupanga kumapiri anga onse, ati Ambuye Yehova, munthu aliyense lupanga lake lidzaombana nalo la mbale wake.


Ndipo mazana atatuwa anaomba malipenga, ndipo Yehova anakanthanitsa yense mnzake ndi lupanga m'misasa monse; ndi a m'misasa anathawa mpaka ku Betesita ku Zerera, mpaka ku malire a Abele-Mehola pa Tabati.


Ndipo ozonda a Saulo ku Gibea wa ku Benjamini anayang'ana; ndipo, onani, khamu la anthu linamwazikana, kulowa kwina ndi kwina.


Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa