Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 12:24 - Buku Lopatulika

24 Koma mumuope Yehova, ndi kumtumikira koona, ndi mtima wanu wonse; lingalirani zinthu zazikuluzo Iye anakuchitirani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Koma mumuope Yehova, ndi kumtumikira koona, ndi mtima wanu wonse; lingalirani zinthu zazikuluzo Iye ana ku chitirani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Muzingoopa Chauta, ndipo muzimtumikira mokhulupirika ndi mtima wanu wonse. Nthaŵi zonse muziganizira zazikulu zimene wakhala akukuchitirani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Koma onetsetsani kuti mukuopa Yehova ndi kumutumikira mokhulupirika ndi mtima wanu wonse. Nthawi zonse muziganizira zinthu zazikulu wakhala akukuchitirani.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 12:24
17 Mawu Ofanana  

koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m'dzanja la adani anu onse.


Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.


Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.


Mtima wanga ukhale wangwiro m'malemba anu; kuti ndisachite manyazi.


Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.


Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa; opusa anyoza nzeru ndi mwambo.


Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.


Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m'maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa machitidwe a manja ake.


Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!


Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.


Iye ndiye lemekezo lanu, Iye ndiye Mulungu wanu, amene anachita nanu zazikulu ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu.


Awa ndi mau a chipangano chimene Yehova analamulira Mose achichite ndi ana a Israele m'dziko la Mowabu, pamodzi ndi chipanganocho anachita nao mu Horebu.


Ndipo Mose anaitana Israele wonse, nati nao, Munapenya inu zonse zimene Yehova anachitira Farao, ndi anyamata ake onse, ndi dziko lake lonse, pamaso panu m'dziko la Ejipito;


Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.


Ndipo tsopano, opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi woona; nimuchotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija la mtsinje, ndi mu Ejipito; nimutumikire Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa