Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Mbiri 2:4 - Buku Lopatulika

4 Ndi Tamara mpongozi wake anambalira Perezi ndi Zera. Ana aamuna onse a Yuda ndiwo asanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndi Tamara mpongozi wake anambalira Perezi ndi Zera. Ana amuna onse a Yuda ndiwo asanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mpongozi wake Tamara nayenso adamubalira Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mpongozi wake Tamara anamuberekera Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 2:4
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wake.


Ana a Perezi: Hezironi, ndi Hamuli.


Ana a Yuda: Perezi, Hezironi, ndi Karimi, ndi Huri, ndi Sobala.


Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, wa ana a Perezi mwana wa Yuda.


Ndi a ana a Zera: Yeuwele ndi abale ao mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi anai.


Ndi Petahiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa milandu yonse ya anthuwo.


Ndipo mu Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, wa ana a Perezi;


Zera, ndiye kholo la banja la Azera; Shaulo, ndiye kholo la banja la Ashaulo.


ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;


mwana wa Aminadabu, mwana wa Admini, mwana wa Arini, mwana wa Hezironi, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda,


ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamara anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu.


Iyo ndiyo mibadwo ya Perezi; Perezi anabala Hezironi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa