Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 7:34 - Buku Lopatulika

34 Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m'thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mwamuna wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 ndipo chifukwa ichi amatanganidwa kwambiri. Mkazi wosakwatiwa kapena namwali, amalabadira za Ambuye. Cholinga chake ndi kudzipereka kwa Ambuye mʼthupi ndi mu uzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amalabadira za dziko lapansi lino, mmene angakondweretsere mwamuna wake.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 7:34
16 Mawu Ofanana  

chifukwa ali wolipidwa, ndipo sasamala nkhosa.


ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.


Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.


koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake.


Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa.


Popanda zakunjazo pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, chalabadiro cha Mipingo yonse.


Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.


monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.


Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu?


Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.


Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a ntchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa