1 Akorinto 7:14 - Buku Lopatulika14 Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Pakuti mwamuna wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mkazi wakeyo. Nayenso mkazi wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mwamuna wakeyo. Pakadapanda apo, bwenzi ana anu atakhala akunja, koma monga zilirimu, ndi ana a Mulungu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo amayeretsedwa chifukwa cha mkazi wakeyo, ndipo mkazi wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha mwamuna wokhulupirirayo. Kupanda apo ana anu akanakhala odetsedwa, koma mmene zililimu ndi oyeretsedwa. Onani mutuwo |