Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 2:11 - Buku Lopatulika

11 Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Kodi ndani mwa anthu angadziwe maganizo a munthu wina, kupatula mzimu wa munthuyo wokhala mʼkati mwake? Chimodzimodzinso palibe amene adziwa maganizo a Mulungu kupatula Mzimu wa Mulunguyo.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 2:11
8 Mawu Ofanana  

Kodi unamva uphungu wachinsinsi wa Mulungu? Ndipo unadzikokera nzeru kodi?


Mtima udziwa kuwawa kwakekwake; mlendo sadudukira ndi chimwemwe chake.


Mzimu wa munthu ndiwo nyali ya Yehova; usanthula m'kati monse mwa mimba.


Uphungu wa m'mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.


Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzake mau a chidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo:


Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa