Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 13:9 - Buku Lopatulika

9 Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Paja timangodziŵa zinthu mopereŵera, ndipo kulalika kwathunso nkopereŵera,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Pakuti timadziwa zinthu pangʼono chabe ndipo timanenera pangʼono chabe.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 13:9
16 Mawu Ofanana  

Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akuzindikiritsa ndani?


Kudziwa ichi kundiposa ndi kundidabwitsa: Kundikhalira patali, sindifikirako.


Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.


Ndani anakwera kumwamba natsikanso? Ndani wakundika nafumbata mphepo? Ndani wamanga madzi m'malaya ake? Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko? Dzina lake ndani? Dzina la mwanake ndani? Kapena udziwa.


Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana, koma Atate yekha, ndi palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.


Pakuti anadziwitsa ndani mtima wake wa Ambuye? Kapena anakhala phungu wake ndani?


Koma pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe.


Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.


koma monga kulembedwa, Zimene diso silinazione, ndi khutu silinazimve, nisizinalowe mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.


Ngati wina ayesa kuti adziwa kanthu sanayambe kudziwa monga ayenera kudziwa.


Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;


Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa