1 Akorinto 13:12 - Buku Lopatulika12 Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Tsopano timaona zinthu ngati m'galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthaŵiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera, koma pa nthaŵiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziŵira ine kotheratu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Pakuti tsopano tiona zinthu mosaoneka bwino ngati mʼgalasi loonera; kenaka tidzaziona maso ndi maso. Tsopano ndidziwa mosakwanira koma kenaka ndidzadziwa mokwanira, monga mmene Mulungu akundidziwira ine. Onani mutuwo |