Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 11:7 - Buku Lopatulika

7 Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Kwa mwamuna palibe chifukwa choti azivalira kanthu kumutu, pakuti amaonetsa maonekedwe ndi ulemerero wa Mulungu. Koma mkazi amaonetsa ulemerero wa mwamuna.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mwamuna sayenera kuphimba kumutu popeza ndi chifaniziro ndi ulemerero wa Mulungu; pamene mkazi ndi ulemerero wa mwamuna.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 11:7
10 Mawu Ofanana  

Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.


Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'chifanizo cha Mulungu;


Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.


Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu; mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake;


Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake; koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo.


Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.


Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde.


Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu.


Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa