Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 11:5 - Buku Lopatulika

5 Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Koma mkazi akamapemphera kapena kulalika mau a Mulungu, osavala kanthu kumutu, akunyoza mutu wake. Kuteroko sikusiyana ndi kungometa mpala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndipo mkazi aliyense wopemphera kapena kunenera asanaphimbe mutu wake sakulemekeza mutu wakewo. Kuli chimodzimodzi kumeta mutu wake.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 11:5
8 Mawu Ofanana  

Tenga mipero, nupere ufa; chotsa chophimba chako, vula chofunda, kwinda m'mwendo, oloka mitsinje.


Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake,


Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu aamuna, ndi aakazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto;


Ndipo munthuyu anali nao ana aakazi anai, anamwali, amene ananenera.


Mwamuna yense woveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wake.


Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde.


Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.


pamenepo mufike naye kwanu kunyumba yanu; ndipo amete tsitsi la pamutu pake, ndi kuwenga makadabo ake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa