Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 1:20 - Buku Lopatulika

20 Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitse nzeru ya dziko lapansi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitsa nzeru ya dziko lapansi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Nanga ali kuti anthu anzeru? Ali kuti aphunzitsi a Malamulo a Mose? Ali kuti anthu onyadira nzeru zamakono zapansipano? Monga Mulungu sadaonetse kuti kudalira nzeru zapansipano nkopusa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Munthu wanzeru ali kuti? Munthu wozama ndi maphunziro ali kuti? Munthu wodziwa zakuya zamakono ali kuti? Kodi Mulungu sanazipusitse nzeru za dziko lapansi?

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 1:20
28 Mawu Ofanana  

Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.


Ndipo uphungu wa Ahitofele anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofele unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu yemwe.


Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.


Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.


Apita nao maphungu atawafunkhira, napulukiritsa oweruza milandu.


Amchotsera wokhulupirika kunena kwake. Nalanda luntha la akulu.


Awachotsera akulu a anthu a padziko mtima wao, nawasokeretsa m'chipululu chopanda njira.


Mtima wako udzaganizira zoopsa; mlembi ali kuti? Ali kuti iye amene anayesa msonkho? Ali kuti iye amene anawerenga nsanja?


Ndine amene nditsutsa zizindikiro za matukutuku, ndi kuchititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao:


Ndani wamvera uthenga wathu? Ndi mkono wa Yehova wavumbulukira yani?


Wosaopa Inu ndani, Mfumu ya amitundu? Pakuti kukuopani ndi kwanu; pakuti mwa anzeru onse a amitundu, ndi m'maufumu ao onse, mulibe akunga Inu.


Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.


Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano.


Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.


Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;


Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;


Pakuti kulembedwa, Ndidzaononga nzeru za anzeru, ndi kuchenjera kwa ochenjera ndidzakutha.


Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai;


koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu;


ndipo zopanda pake za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; kuti akathere zinthu zoti ziliko;


Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.


Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi ino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi ino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;


imene saidziwa mmodzi wa akulu a nthawi ya pansi pano: pakuti akadadziwa sakadapachika Mbuye wa ulemerero;


Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m'nthawi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru.


Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao;


Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa?


Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa