Ndipo inu, gulu langa, atero Ambuye Yehova, ndiweruza pakati pa zoweta ndi zoweta, nkhosa zamphongo ndi atonde.
Yuda 1:22 - Buku Lopatulika Ndipo ena osinkhasinkha muwachitire chifundo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ena osinkhasinkha muwachitire chifundo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pali ena amene ali okayika, amenewo muziŵachitira chifundo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muwachitire chifundo amene akukayika. |
Ndipo inu, gulu langa, atero Ambuye Yehova, ndiweruza pakati pa zoweta ndi zoweta, nkhosa zamphongo ndi atonde.
koma mwenzi nditakhala nanu tsopano, ndi kusintha mau anga; chifukwa ndisinkhasinkha nanu.
Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.
mudzisunge nokha m'chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kufikira moyo wosatha.
koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwachitire chifundo ndi mantha, nimudane naonso malaya ochitidwa mawanga ndi thupi.