Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo;
Yuda 1:10 - Buku Lopatulika Koma iwowa zimene sazidziwa azichitira mwano; ndipo zimene azizindikira chibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iwowa zimene sazidziwa azichitira mwano; ndipo zimene azizindikira chibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma anthu ameneŵa amachita chipongwe zinthu zimene sazidziŵa. Ndipo zinthu zimene amazidziŵa ndi nzeru zachibadwa, zonga za nyama, ndizo zimene zimaŵaononga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ndipo zinthu zimene amazidziwa ndi nzeru zachibadwa, monga za nyama, ndizo zimene zimawawononga. |
Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo;
chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.
Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,