Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu.
Yohane 3:4 - Buku Lopatulika Nikodemo ananena kwa Iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amake ndi kubadwa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nikodemo ananena kwa Iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amake ndi kubadwa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nikodemo adamufunsa kuti, “Kodi munthu angathe kubadwanso bwanji atakalamba kale? Kodi nkukaloŵa m'mimba mwa amai ake kuti abadwe kachiŵiri?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?” |
Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu.
Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.
Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.
Pamenepo ambiri a ophunzira ake, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?
Pakuti mau a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.
Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sangathe kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.