Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.
Yohane 15:3 - Buku Lopatulika Mwakhala okonzeka tsopano inu chifukwa cha mau amene ndalankhula ndi inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwakhala okonzeka tsopano inu chifukwa cha mau amene ndalankhula ndi inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mwayera kale chifukwa cha mau amene ndakuuzani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ndayankhula inu. |
Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.
Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka.
Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi.
Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;