Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Obadiya 1:8 - Buku Lopatulika

Ati Yehova, Kodi sindidzaononga tsiku lija anzeru mwa Edomu, ndi luntha m'phiri la Esau?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ati Yehova, Kodi sindidzaononga tsiku lija anzeru mwa Edomu, ndi luntha m'phiri la Esau?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta akuti, “Nthaŵi imeneyo ndidzaononga anzeru onse a ku Edomu, ndidzathetsa kuchenjera konse kwa zidzukulu za Esau.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yehova akunena kuti, “Tsiku limenelo, kodi sindidzawononga anthu onse anzeru a ku Edomu, anthu odziwa zinthu mʼmapiri a Esau?

Onani mutuwo



Obadiya 1:8
8 Mawu Ofanana  

Yehova aphwanya upo wa amitundu, asandutsa chabe zolingirira za mitundu ya anthu.


Akalonga a Zowani apusa ndithu; uphungu wa aphungu anzeru a Farao wasanduka wopulukira; bwanji iwe unena kwa Farao, Ine ndine mwana wa anzeru, mwana wa mafumu akale?


Nanga tsopano anzeru ali kuti? Akuuze iwe tsopano; adziwe chimene Yehova wa makamu watsimikiza mtima kuchitira Ejipito.


Ndipo mzimu wa Ejipito adzakhala wachabe pakati pake; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wake; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.


chifukwa chake, taonani, ndidzachitanso mwa anthu awa ntchito yodabwitsa, ngakhale ntchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu ao anzeru idzatha, ndi luntha la anthu ao ozindikira lidzabisika.