Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska.
Numeri 9:4 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, kuti achite Paska. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, kuti achite Paska. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Mose adauza Aisraele kuti azichita Paska. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Mose anawuza Aisraeli kuti azichita Paska, |
Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska.
Tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, muziuchita, pa nyengo yake yoikidwa; muuchite monga mwa malemba ake onse, ndi maweruzo ake onse.
Ndipo anachita Paska mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo m'chipululu cha Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israele anachita.