Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 7:87 - Buku Lopatulika

ng'ombe zonse za nsembe yopsereza ndizo ng'ombe khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziwiri, anaankhosa a chaka chimodzi khumi ndi awiri, pamodzi ndi nsembe yao yaufa; ndi atonde a nsembe zauchimo khumi ndi awiri;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ng'ombe zonse za nsembe yopsereza ndizo ng'ombe khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziwiri, anaankhosa a chaka chimodzi khumi ndi awiri, pamodzi ndi nsembe yao yaufa; ndi atonde a nsembe zauchimo khumi ndi awiri;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyama zonse zoperekera nsembe zopsereza zinali ng'ombe zamphongo khumi ndi ziŵiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziŵiri, anaankhosa amphongo a chaka chimodzi khumi ndi aŵiri, pamodzi ndi chopereka cha chakudya, ndiponso atonde khumi ndi aŵiri operekera nsembe zopepesera machimo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yopsereza chinali motere: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, nkhosa zazimuna khumi ndi ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi awiri a chaka chimodzi pamodzi ndi chopereka chachakudya. Mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri zinali za nsembe yopepesera machimo.

Onani mutuwo



Numeri 7:87
2 Mawu Ofanana  

Zipande zagolide ndizo khumi ndi ziwiri, zodzala ndi chofukiza, chipande chonse masekeli khumi, kuyesa sekeli wa malo opatulika; golide wonse wa zipandezo ndiwo masekeli zana limodzi ndi makumi awiri;


ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, anaankhosa a chaka chimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka chiperekere, litadzozedwa guwa la nsembe.