Numeri 7:47 - Buku Lopatulika ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuwele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuwele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Eliyasafu mwana wa Deuwele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuweli. |