Numeri 7:36 - Buku Lopatulika Tsiku lachisanu kalonga wa ana a Simeoni, ndiye Selumiele, mwana wa Zurishadai: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku lachisanu kalonga wa ana a Simeoni, ndiye Selumiele, mwana wa Zurishadai: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lachisanu linali la Selumiele mwana wa Zurishadai, mtsogoleri wa Asimeoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku lachisanu Selumieli mwana wa Zurisadai, mtsogoleri wa fuko la Simeoni, anabweretsa chopereka chake. |
Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Simeoni; ndi kalonga wa ana a Simeoni ndiye Selumiele mwana wa Zurishadai.
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Elizuri mwana wa Sedeuri.
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;