Numeri 5:31 - Buku Lopatulika Mwamunayo ndiye wosachita mphulupulu, koma mkazi uyo asenze mphulupulu yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwamunayo ndiye wosachita mphulupulu, koma mkazi uyo asenze mphulupulu yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwamuna adzakhala wopanda tchimo lililonse, koma mkazi ndiye adzasenza tchimo lake.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwamunayo adzakhala wopanda tchimo lililonse, koma mkaziyo adzasenza zotsatira za tchimo lake.’ ” |
Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.
Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.
kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo achitira mkazi wake nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amchitire chilamulo ichi chonse.
Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.