ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti achitire nsanje mkazi wake, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amchitire mkazi wake nsanje angakhale sanadetsedwe;
Numeri 5:30 - Buku Lopatulika kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo achitira mkazi wake nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amchitire chilamulo ichi chonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo achitira mkazi wake nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amchitire chilamulo ichi chonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kapena mwamuna akayamba kuchitira mkazi wake nsanje ndipo akumganizira zoipa. Mwamunayo amuimike mkazi wake pamaso pa Chauta, ndipo wansembe amchitire monga momwe lamulo likunenera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kapena pamene maganizo a nsanje abwera kwa mwamuna wake chifukwa chokayikira mkazi wakeyo. Wansembe azitenga mkazi wotere ndi kumuyimiritsa pamaso pa Yehova ndipo agwiritse ntchito lamulo lonseli kwa mkaziyo. |
ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti achitire nsanje mkazi wake, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amchitire mkazi wake nsanje angakhale sanadetsedwe;
Ichi ndi chilamulo cha nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wake, ampatukira nadetsedwa;