Chomwecho njira ya mkazi wachigololo; adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinachite zoipa.
Numeri 5:13 - Buku Lopatulika ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wake, ndi kumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwire alimkuchita; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wake, ndi kumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwire alimkuchita; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwamuna wina atachita naye chigololo, zimenezo zitha kubisika, mwamuna wake osazidziŵa. Mkaziyo atha kukhala wosazindikirika kuti wadziipitsa, chifukwa chosoŵa mboni yomtsutsa, popeza kuti sadampezerere akuchita kumene. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero nakagonana ndi mwamuna wina koma mwamuna wake wosadziwa, ndipo palibe wina aliyense wadziwa za kudzidetsa kwake (pakuti palibe mboni yomuneneza chifukwa sanagwidwe akuchita), |
Chomwecho njira ya mkazi wachigololo; adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinachite zoipa.
Mumatama lupanga lanu, mumachita chonyansa, mumaipsa yense mkazi wa mnansi wake; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?
Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.