Numeri 5:12 - Buku Lopatulika Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mkazi wamwini akapatukira mwamuna wake, nakamchitira mosakhulupirika, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mkazi wa mwini akapatukira mwamuna wake, nakamchitira mosakhulupirika, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Uza Aisraele kuti, mwina mkazi adzazembera mwamuna wake namachita zosakhulupirika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mkazi wa munthu wina ayenda njira yosayenera nakhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake, |
Ichi ndi chilamulo cha nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wake, ampatukira nadetsedwa;
Munthu akatenga mkazi akhale wake, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pake, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata ya chilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lake, ndi kumtulutsa m'nyumba mwake.