Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 4:7 - Buku Lopatulika

Ndi pa gome la mkate woonekera ayale nsalu yamadzi, naikepo mbale zake, ndi zipande, ndi mitsuko, ndi zikho zakuthira nazo; mkate wa chikhalire uzikhalaponso.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndi pa gome la mkate woonekera ayale nsalu yamadzi, naikepo mbale zake, ndi zipande, ndi mitsuko, ndi zikho zakuthira nazo; mkate wa chikhalire uzikhalaponso.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ayale nsalu yobiriŵira pa tebulo la buledi wokhala pamenepo nthaŵi zonse, ndi kuikapo mbale zake, zipande zake zotapira lubani, mabeseni ake, ndi zikho za chopereka cha chakumwa. Aikeponso buledi wokhala pamenepo nthaŵi zonse.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Pa tebulo pamene pamakhala buledi wa ansembe aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo, ndipo aziyikapo mbale, mabeseni, zipande ndi mitsuko yoperekera nsembe yachakumwa. Aziyikaponso buledi wokhala pamenepo nthawi zonse.

Onani mutuwo



Numeri 4:7
5 Mawu Ofanana  

Ndipo ayale pa izi nsalu yofiira, ndi kuliphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.


Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.