Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo chiwerengo chao kuwawerenga mmodzimmodzi ndicho amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu.
Numeri 4:46 - Buku Lopatulika Owerengedwa onse a Alevi, amene Mose ndi Aroni ndi akalonga a Israele anawawerengera, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Owerengedwa onse a Alevi, amene Mose ndi Aroni ndi akalonga a Israele anawawerengera, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Mose ndi Aroni, pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele, adaŵaŵerenga Alevi onsewo potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Mose, Aaroni ndi atsogoleri a Israeli anawerenga Alevi onse monga mwa mafuko ndi mabanja awo. |
Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo chiwerengo chao kuwawerenga mmodzimmodzi ndicho amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu.
ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mu udikiro mwao, monga mwa zigawo zao;
Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.
kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa kugwira ntchito ya utumikiwu, ndiyo ntchito ya akatundu m'chihema chokomanako;