Numeri 4:29 - Buku Lopatulika Kunena za ana a Merari, Uwawerenge monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kunena za ana a Merari, Uwawerenge monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Uŵerenge ana a Merari potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Werenga Amerari monga mwa mafuko awo ndi mabanja awo. |
Iyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Geresoni m'chihema chokomanako; ndipo Itamara mwana wa Aroni wansembe ayang'anire udikiro wao.
Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuchita ntchito ya chihema chokomanako.
napatsa ana a Merari magaleta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa ntchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe.