Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 4:27 - Buku Lopatulika

Ntchito yonse ya ana a Ageresoni, kunena za akatundu ao ndi ntchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ake aamuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ntchito yonse ya ana a Ageresoni, kunena za akatundu ao ndi ntchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ake amuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Amene aziyang'anira ntchito zonse za ana a Ageresoni, ndi Aroni pamodzi ndi ana ake. Aziyang'anira zonse zimene ayenera kunyamula, ndi zonse zimene ayenera kuchita. Ndinu amene mudzayenera kuŵafotokozera udindo wa kunyamula zonse zija.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ntchito yawo yonse, kaya kunyamula kapena kugwira ntchito zina, achite Ageresoni motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Uwagawire ntchito zonse zimene akuyenera kugwira.

Onani mutuwo



Numeri 4:27
4 Mawu Ofanana  

ndi nsalu zotchingira za pabwalo, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo lili pa chihema ndi paguwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za ntchito zao, ndi zonse achita nazo; m'menemo muli ntchito zao.


Iyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Geresoni m'chihema chokomanako; ndipo Itamara mwana wa Aroni wansembe ayang'anire udikiro wao.


Monga Iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ake oyera mtima, akale lomwe,


Ndipo ndikutamandani kuti m'zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.