Nafa Eleazara wopanda ana aamuna, koma ana aakazi ndiwo; ndi asuweni ao ana a Kisi anawatenga akhale akazi ao.
Numeri 36:8 - Buku Lopatulika Ndipo mwana wamkazi yense wa mafuko a ana a Israele, wakukhala nacho cholowa, akwatibwe ndi wina wa banja la fuko la kholo lake, kuti ana a Israele akhale nacho yense cholowa cha makolo ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mwana wamkazi yense wa mafuko a ana a Israele, wakukhala nacho cholowa, akwatibwe ndi wina wa banja la fuko la kholo lake, kuti ana a Israele akhale nacho yense cholowa cha makolo ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mkazi aliyense amene alandira choloŵa m'fuko lililonse la Aisraele, akwatiwe ndi ana a abale a bambo wao. Mwisraele aliyense adzalandira choloŵa cha makolo ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwana wamkazi aliyense amene adzalandira cholowa cha dziko la fuko lililonse la Israeli ayenera kukwatiwa ndi munthu wa fuko la abambo ake. |
Nafa Eleazara wopanda ana aamuna, koma ana aakazi ndiwo; ndi asuweni ao ana a Kisi anawatenga akhale akazi ao.
Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko, pakuti mafuko a ana a Israele adzamamatira lonse ku cholowa chakechake.