Ana aakazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao.
Numeri 36:5 - Buku Lopatulika Ndipo Mose analamulira ana a Israele monga mwa mau a Yehova, nati, Fuko la ana a Yosefe linena zoona. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose analamulira ana a Israele monga mwa mau a Yehova, nati, Fuko la ana a Yosefe linena zoona. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Mose adaŵalamula Aisraele potsata mau a Chauta, adati, “Zimene akunena ana a Yosefezi nzoona. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono mwa lamulo la Yehova, Mose anapereka lamulo ili kwa Aisraeli: “Zimene ana a Yosefe akunena ndi zoona. |
Ana aakazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao.
Ndipo pofika chaka choliza cha ana a Israele adzaphatikiza cholowa chao ku cholowa cha fuko limene akhalako; chotero adzachotsa cholowa chao ku cholowa cha fuko la makolo athu.
Cholamulira Yehova za ana aakazi a Zelofehadi ndi ichi, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ake; komatu akwatibwe nao a banja la fuko la makolo ao okhaokha.
Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, pamene munanena ndi ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Ndidamva mau a kunena kwao kwa anthu awa, amene ananena ndi iwe; chokoma chokhachokha adanenachi.