Numeri 32:17 - Buku Lopatulika koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israele, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao; ndi ang'ono athu adzakhala mizinda ya malinga chifukwa cha okhala m'dzikomo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israele, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao; ndi ang'ono athu adzakhala m'midzi ya malinga chifukwa cha okhala m'dzikomo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake tidzatenga zida zankhondo ndi kutsogolera Aisraele mpaka titakaŵafikitsa ku malo ao. Koma ana athu adzakhala m'mizinda yamalinga, chifukwa choopa anthu a m'dziko muno. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ndife okonzeka kutenga zida za nkhondo ndi kupita pamodzi ndi Aisraeli mpaka titakawafikitsa ku malo awo. Panopa, akazi ndi ana athu akhala mʼmizinda yotetezedwa, kuwateteza kwa anthu okhala mʼdzikoli. |