Asadzitengere mkazi wachigololo, kapena woipsidwa; asatenge mkazi woti adamchotsa mwamuna wake; popeza apatulikira Mulungu wake.
Numeri 30:9 - Buku Lopatulika Koma chowinda cha mkazi wamasiye, kapena mkazi wochotsedwa, zilizonse anamanga nazo moyo wake zidzamkhazikikira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma chowinda cha mkazi wamasiye, kapena mkazi wochotsedwa, zilizonse anamanga nazo moyo wake zidzamkhazikikira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mkazi wamasiye kapena wosudzulidwa akalumbira kapena kulonjeza kuti adzachita kanthu kalikonse, ayenera kukachitadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Mayi wamasiye kapena wosiyidwa ukwati akalumbira kapena kulonjeza kuti adzachita kanthu kalikonse, ayenera kukachitadi. |
Asadzitengere mkazi wachigololo, kapena woipsidwa; asatenge mkazi woti adamchotsa mwamuna wake; popeza apatulikira Mulungu wake.
Ndipo ngati anawinda m'nyumba ya mwamuna wake, kapena anamanga moyo wake ndi chodziletsa ndi kulumbirapo,
Koma mwamuna wake akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza chowinda chake anali nacho, ndi zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; ndipo Yehova adzamkhululukira.
zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.
Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.