Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
Numeri 30:8 - Buku Lopatulika Koma mwamuna wake akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza chowinda chake anali nacho, ndi zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; ndipo Yehova adzamkhululukira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mwamuna wake akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza chowinda chake anali nacho, ndi zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; ndipo Yehova adzamkhululukira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ngati pa tsiku limene mwamunayo wamva zimenezo, amkaniza, pamenepo ammasula mkaziyo kwa zimene adalumbira ndi kwa zimene adalankhula mosaganiza bwino, ndipo Chauta adzamkhululukira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati mwamuna wake amuletsa atamva kulumbira kwakeko, pamenepo amumasula mayiyo ku zimene analumbira komanso ku zimene analonjeza mosaganiza bwinozo ndipo Yehova adzamukhululukira. |
Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
Ndipo pamene tinafukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira nsembe zothira, kodi tinamuumbira iye mikate yakumpembedzera, ndi kumthirira nsembe zothira, opanda amuna athu?
kapena munthu akalumbira ndi milomo yake osalingirira kuchita choipa, kapena kuchita chabwino, chilichonse munthu akalumbira osalingirira, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula chimodzi cha izi:
Koma atate wake akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zake zonse, ndi zodziletsa zake zonse anamanga nazo moyo wake, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wake anamletsa.
nakazimva mwamuna wake, nakakhala naye chete tsiku lakuzimva iye; pamenepo zowinda zake zidzakhazikika, ndi zodziletsa anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.
Koma chowinda cha mkazi wamasiye, kapena mkazi wochotsedwa, zilizonse anamanga nazo moyo wake zidzamkhazikikira.
Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.
Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye.
Ndipo Elikana mwamuna wake anati, Chita chimene chikukomera nukhale kufikira utamletsa kuyamwa; komatu Yehova akhazikitse mau ake. Chomwecho mkaziyo anakhala nayamwitsa mwana wake, kufikira anamletsa kuyamwa.