ndipo mwamuna wake anamva, koma anakhala naye chete osamletsa, pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi zodziletsa zonse anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.
Numeri 30:10 - Buku Lopatulika Ndipo ngati anawinda m'nyumba ya mwamuna wake, kapena anamanga moyo wake ndi chodziletsa ndi kulumbirapo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ngati anawinda m'nyumba ya mwamuna wake, kapena anamanga moyo wake ndi chodziletsa ndi kulumbirapo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mkazi wokwatiwa akalonjeza nalumbira kuti adzachitadi zimene walonjeza, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Koma ngati mayi wokwatiwa alumbira nalonjeza kuti adzachitadi zimene walonjeza, |
ndipo mwamuna wake anamva, koma anakhala naye chete osamletsa, pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi zodziletsa zonse anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.
Munthu akachitira Yehova chowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wake chodziletsa, asaipse mau ake; azichita monga mwa zonse zotuluka m'kamwa mwake.
Koma chowinda cha mkazi wamasiye, kapena mkazi wochotsedwa, zilizonse anamanga nazo moyo wake zidzamkhazikikira.
Ndipo Elikana mwamuna wake anati, Chita chimene chikukomera nukhale kufikira utamletsa kuyamwa; komatu Yehova akhazikitse mau ake. Chomwecho mkaziyo anakhala nayamwitsa mwana wake, kufikira anamletsa kuyamwa.