ndiponso ansembe a fuko la Levi sadzasowa munthu pamaso panga wakupereka nsembe zopsereza, ndi kutentha nsembe zaufa, ndi wakuchita nsembe masiku onse.
Numeri 3:5 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anati kwa Mose, |
ndiponso ansembe a fuko la Levi sadzasowa munthu pamaso panga wakupereka nsembe zopsereza, ndi kutentha nsembe zaufa, ndi wakuchita nsembe masiku onse.
Koma adzakhala atumiki m'malo anga opatulika, akuyang'anira kuzipata za Kachisi, ndi kutumikira mu Kachisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera, naime pamaso pao kuwatumikira.
Ndiponso abale ako, fuko la Alevi, fuko la kholo lako, uwayandikizitse pamodzi ndi iwe, kuti aphatikane ndi iwe, ndi kukutumikira; koma iwe ndi ana ako pamodzi ndi iwe mukhale ku khomo la chihema cha mboni.
Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.
ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yochokera kwa ana a Israele, kuti akhale akuchita ntchito ya Yehova.