Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 29:9 - Buku Lopatulika

ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodziyo;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a efa wa ng'ombe, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodziyo;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo mupereke chopereka cha chakudya chosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongoyo, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri;

Onani mutuwo



Numeri 29:9
4 Mawu Ofanana  

Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta.


limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri;


koma mubwere nayo nsembe yopsereza kwa Yehova, ya fungo lokoma; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;