ndi pa mwanawankhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira.
Numeri 28:13 - Buku Lopatulika ndi limodzi la magawo khumi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ikhale nsembe yaufa, ndiwo wa mwanawankhosa yense; ndiyo nsembe yopsereza ya fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi limodzi la magawo khumi la ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndiwo wa mwanawankhosa yense; ndiyo nsembe yopsereza ya fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndiponso kilogaramu limodzi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa mwanawankhosa aliyense. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza yotulutsa fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo pa mwana wankhosa aliyense, chopereka cha ufa wa kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, izi ndi za nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto ya kwa Yehova. |
ndi pa mwanawankhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira.
Kapena ukonzere nkhosa yamphongo nsembe yaufa, awiri mwa magawo khumi a efa wa ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta, limodzi la magawo atatu la hini.
ndi atatu a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndiwo wa ng'ombe iliyonse; ndi awiri a magawo khumi a ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndiwo wa nkhosa yamphongo imodziyo;
Ndipo nsembe zake zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la hini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwanawankhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse kunena miyezi yonse ya chaka.