Ana aakazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao.
Numeri 27:8 - Buku Lopatulika Ndipo unene ndi ana a Israele, ndi kuti, Akafa munthu wamwamuna wopanda mwana wamwamuna, cholowa chake achilandire mwana wake wamkazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo unene ndi ana a Israele, ndi kuti, Akafa munthu wamwamuna wopanda mwana wamwamuna, cholowa chake achilandire mwana wake wamkazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo uŵauze Aisraele kuti, ‘Munthu akafa opanda mwana wamwamuna, choloŵa chake chikhale cha mwana wake wamkazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Uza Aisraeli kuti, ‘Ngati munthu afa wosasiya mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi. |
Ana aakazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao.