Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.
Numeri 27:12 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kwera m'phiri ili la Abarimu, nupenye dziko limene ndapatsa ana a Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kwera m'phiri ili la Abarimu, nupenye dziko limene ndapatsa ana a Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose kuti, “Ukwere phiri ili la Abarimu, kuti uwone dziko limene ndapatsa Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Kwera phiri la Abarimu kuti ukaone dziko limene ndalipereka kwa Aisraeli. |
Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.
Kwera ku Lebanoni, nufuule; kweza mau ako mu Basani; nufuule mu Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'chihema chokomanako.