Yeremiya 22:20 - Buku Lopatulika20 Kwera ku Lebanoni, nufuule; kweza mau ako mu Basani; nufuule mu Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Kwera ku Lebanoni, nufuule; kweza mau ako m'Basani; nufuule m'Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 “Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, kwerani ku mapiri ku Lebanoni, mukalire mofuula kumeneko, mau anu amveke mpaka ku Basani. Mulire mofuula muli ku Abarimu, chifukwa onse amene munkaŵadalira aonongeka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 “Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, pitani ku mapiri a Lebanoni kuti mukalire mofuwula kumeneko, mawu anu akamveke mpaka ku Basani. Mulire mofuwula muli ku Abarimu chifukwa abwenzi ako onse awonongeka. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.