Numeri 26:9 - Buku Lopatulika Ndi ana a Eliyabu: Nemuwele, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, muja anatsutsana ndi Yehova; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi ana a Eliyabu: Nemuwele, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, muja anatsutsana ndi Yehova; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo ana a Eliyabu anali Nemuwele, Datani ndi Abiramu. Ameneŵa anali omwe aja amene adasankhidwa mu mpingo, amenenso adakangana ndi Mose ndi Aroni pogwirizana ndi Kora, pamene adatsutsana ndi Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova. |
Iwo ndiwo oitanidwa a khamu, akalonga a mafuko a makolo ao; ndiwo akulu a zikwizo za Israele.
Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.