Ndipo masiku asanu ndi awiri a chikondwerero akonzere Yehova nsembe yopsereza, ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri zopanda chilema, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiriwa; ndi tonde tsiku ndi tsiku, akhale wa nsembe yauchimo.
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Ndimangireni kuno maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere kuno ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.
Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Mundimangire pano maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere pano ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo chimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera.