Pamenepo Balamu anati kwa bulu, Chifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m'dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe.
Numeri 22:30 - Buku Lopatulika Ndipo bulu anati kwa Balamu, Si ndine bulu wako amene umayenda wokwera pa ine chiyambire ndili wako kufikira lero lino? Kodi ndikakuchitira chotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo bulu anati kwa Balamu, Si ndine bulu wako amene umayenda wokwera pa ine chiyambire ndili wako kufikira lero lino? Kodi ndikakuchitira chotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Buluyo adafunsanso Balamu kuti, “Kodi sindine bulu wanu amene mwakhala mukundikwera moyo wanu wonse mpaka lero lino? Kodi zimenezi ndidakuchitiranipo nkale lonse?” Balamu adayankha kuti “Iyai.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Buluyo anati kwa Balaamu, “Kodi sindine bulu wanu, amene mumakwera nthawi zonse kufikira lero? Kodi ndinakuchitiranipo zoterezi?” Iye anati “Ayi.” |
Pamenepo Balamu anati kwa bulu, Chifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m'dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe.
Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola lili kudzanja, ndipo anawerama mutu wake, nagwa nkhope yake pansi.
koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyaluka kwa mneneriyo.